Ezra 2

Mʼndandanda wa Ayuda amene Anabwerera

1Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake.
2
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana).

Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:

 3Zidzukulu za Parosi 2,172
 4zidzukulu za Sefatiya 372
 5zidzukulu za Ara 775
 6zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu) 2,812
 7zidzukulu za Elamu 1,254
 8zidzukulu za Zatu 945
 9zidzukulu za Zakai 760
 10zidzukulu za Bani 642
 11zidzukulu za Bebai 623
 12zidzukulu za Azigadi 1,222
 13zidzukulu za Adonikamu 666
 14zidzukulu za Bigivai 2,056
 15zidzukulu za Adini 454
 16zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 98
 17zidzukulu za Bezayi 323
 18zidzukulu za Yora 112
 19zidzukulu za Hasumu 223
 20zidzukulu za Gibari 95.

20
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.

 21Anthu a ku Betelehemu 123
 22Anthu aamuna a ku Netofa 56
 23Anthu aamuna a ku Anatoti 128
 24Anthu aamuna a ku Azimaveti 42
 25Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti 743
 26Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba 621
 27Anthu aamuna a ku Mikimasi 122
 28Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai 223
 29Anthu aamuna a ku Nebo 52
 30Anthu aamuna a ku Magaibisi 156
 31Anthu aamuna a ku Elamu wina 1,254
 32Anthu aamuna a ku Harimu 320
 33Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono 725
 34Anthu aamuna a ku Yeriko 345
 35Anthu aamuna a ku Sena 3,630.


36
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Ansembe anali awa:

   Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa) 973
 37Zidzukulu za Imeri 1,052
 38Zidzukulu za Pasuri 1,247
 39Zidzukulu za Harimu 1,017.


40Alevi anali awa:

   Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya)     74.


41Anthu oyimba nyimbo anali awa:

   Zidzukulu za Asafu     128.


42Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

   Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai     139.


43
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za
   Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
 44zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni,
 45zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu,
 46zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani,
 47zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya,
 48zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu,
 49zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai,
 50zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu,
 51zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
 52zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
 53zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema,
 54zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa.


55
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi:

Zidzukulu za
   Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda,
 56zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
 57zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu,
   zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami.
 58Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali 392.


59
In order to format the table contained in this verse correctly, it has been necessary to move the content of some adjacent verses into it.
Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
 60Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali 652.


61Ndi ena pakati pa ansembe anali awa:

Zidzukulu za
   Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.)

62Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. 63Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.

64Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, 65kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. 66Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, 67ngamira 435 ndi abulu 6,720.

68Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. 69Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.

70Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.

Copyright information for NyaCCL